Tuesday, March 5, 2024
Local Malawi News

AMWALIRA ATAMWA MOWA OSADYERA KU BLANTYRE

Bambo wa zaka 48 zakubadwa, Wyson Howa wamwalira atamwa mowa ochuluka koma osadyera.

Izi akuti zachitika pamudzi pa Chibwana ku Chilomoni m’boma la Blantyre.

Malingana ndi wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Blantyre, Aubrey Singanyama, anthu ena anaona Howa akupapila Kachaso Lachiwiri lapitali opanda kudyera.

Singanyama wati mkuluyu anapezeka tsiku lotsatiralo ali thapsaa mnyumba mwake, kutsatira chipikisheni chomwe anthu oyandikana naye anachita, malemuyu atasowa kwa pa khomopo mmawa wa tsikulo.

“Apa, nkhaniyi anakayitula mmanja mwa apolisi ku Chilomoni omwe anatengera thupili ku chipatala cha mderalo kuti akalipime, ndipo zotsatira zinasonyeza kuti Imfa yadza kaamba komwa mowa ochuluka osadyera.

Malemu Wyson Howa anali a mmudzi mwa Stepe, mfumu yayikulu Chimaliro m’boma la Thyolo.

(Visited 15 times, 1 visits today)
admin
the authoradmin
News Breeze Malawi is an independent online news portal which reports news from Malawi, Africa and elsewhere. Our reports are not opinionated and strictly follow the rules and laws of reporting in professional journalism. Contact - newsbreezemalawi@gmail.com

Leave a Reply