Wednesday, February 21, 2024
Local Malawi News

M’BAMBO AMWALIRA ATAMWA KACHASU KU SALIMA

Bambo wina wa zaka 76, m’mudzi wa Kaphinda mfumu yaikulu Kambalame ku Salima wapezeka atafa atamwa kachasu osadyera.

M’neneri wa polisi m’bomali, Jacob Khembo wati malemuwa, Nkhoma Phiri, anali chidakwa chodziwika bwino ndipo m’mawa wa dzulo anapita komwa mowa monga mwachizolowezi koma osadya kalikonse.

A MAN BREWING KACHASU

“Koma madzulo pobwelela kwawo, anagwa panjira. Anthu odutsa ndi omwe anamupeza ndikuwadziwitsa apolisi apa Chipoka za nkhaniyi,” watero Khembo.

Madotolo pa chipatala cha Chipoka komwe atsimikiza kuti malemuwa amwalira chifukwa chokumwa mowa osadya kalikonse.

(Visited 5 times, 1 visits today)
admin
the authoradmin
News Breeze Malawi is an independent online news portal which reports news from Malawi, Africa and elsewhere. Our reports are not opinionated and strictly follow the rules and laws of reporting in professional journalism. Contact - newsbreezemalawi@gmail.com

Leave a Reply