Saturday, March 2, 2024
Local Malawi News

‘MBOLA’ KU MA DEMO AKU LILONGWE

Tsogolo la zionetsero zofuna kukamiza President Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake, Dr. Saulos Chilima ku Lilongwe lero silikuoneka pakadalipano pomwe malo oyambira zionetsero, pa Wakawaka, pali zii ngakhale nthawi yoyambira yadutsa.

Ngakhale izi zili chomwechi, apolisi afika kale mgalimoto zawo pa malowa.

Koma ena mwa akuluakulu omwe akonza dongosololi akuti ziwonetselozi zichitikabe ngakhale anthu sadafikebe.

Mtsogoleri wa bungwe la Centre for Democracy Watch-CEDWAT Levie Luwemba, yemwe wafika pa malowa ku Area 36, akuti apitilira ndi zionetserozi.

Pakadalipano, ntchito zamalonda pa Wakawaka zikupitilila monga mwa nthawi zonse.

Lachisanu, DC wa boma la Lilongwe, Dr. Lawford Palani adaletsa zionetserozi ponena kuti apolisi atangwanika kupereka chitetezo m’malo omwetsera mafuta a galimoto koma dzulo bwalo la milandu ku Lilongwe linati zionetserozi zipitilire lero.

(Visited 6 times, 1 visits today)
admin
the authoradmin
News Breeze Malawi is an independent online news portal which reports news from Malawi, Africa and elsewhere. Our reports are not opinionated and strictly follow the rules and laws of reporting in professional journalism. Contact - newsbreezemalawi@gmail.com

Leave a Reply