Monday, March 4, 2024
Local Malawi News

MFUMU YAMZINDA INJATIDWA KAMBA KOGWILIRA MDZUKULU

Mfumu Yamzinda wa Mzuzu, Gift Desire Nyirenda ayinjata poiganizira kuti yakhala ikugwililira mdzukulu wake wamkazi wa zaka 14.

M’neneri wa polisi ya Mzuzu, Paul Tembo watsimikiza za nkhani-yi ponena kuti izi zidachitika usiku wapa 1 August 2022 ku Nkhorongo ku dera la Luwinga munzindawu.

Gift Desire Nyirenda

Tembo watinso mwanayu, yemwe ali mu Standard 7, amagona limodzi ndi mwana wa a Nyirenda wa mkazi m’nyumba mwawo ngati ankolo ake.

“Mu usikuwu, a Nyirenda adabwera kuchipanda kwa mwanayu kudzathimitsa magetsi kenako adapita. Patapita mphindi zochepa adabweranso kwa mdzukulu wawoyu mkukakamiza kuchita naye zadama atamung’ambira chovala chake chamkati. Ankafuna kuti amupatse mwanayu K2000 koma adakana ndipo adamuopseza kuti akangowulula amupha. Usiku wapa 2 August, adabweranso koma msungwanayu adakana,” watero Tembo mu kalata yomwe watulutsa.

Kalatayi yatinso a Nyirenda, omwe ndi khansala wa chipani cha MCP ku dera la Mzuzu City, akhala akuchita izi kwa mdzukulu wawo-yu kangapo konse.

Tembo wati pakadalipano mwanayu akulandira thandizo ku nthambi ya polisi yoona za anthu ochitiridwa nkhanza.

A Nyirenda akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.

(Visited 21 times, 1 visits today)
admin
the authoradmin
News Breeze Malawi is an independent online news portal which reports news from Malawi, Africa and elsewhere. Our reports are not opinionated and strictly follow the rules and laws of reporting in professional journalism. Contact - newsbreezemalawi@gmail.com

Leave a Reply