Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Saulos Chilima wati ngati pali anthu ena osakondwera ndi mgwirizano wa zipani wa Tonse aneneretu nthawi isanathe kuti mdziko muno muchitikeso zisankho zina.
Chilima wanena izi polankhula ku mtundu wa Malawi Lachisanu munzinda wa Lilongwe.
Malinga ndi a Chilima, mgwirizano-wu unalimbikitsidwa ndi abusa amipingo yosiyana-siyana.
“Anthu ena monga a Lobin Lowe omwe ndi nduna ya za ulimi, malemu Lingison Belekanyama adapempha kuti ndidzichepetse ndikukhara wachiwiri Kwa a Chakwera,” adatero pouza mtundu wa amalawi.
Popitiliza, a Chilima ati ngati anthu ena akufuna kuti mgwirizano wa Tonse uthe, achite izi poitanitsa msonkhano woti akachite zokambirana pa nkhaniyi komaso izi zitanthauza kuti aMalawi akavotenso chifukwa bomali lidakharapo chifukwa Cha mgwirizano.
Poulura zina mwazomwe adagwirizana, a Chilima ati mgwirizano wawo ndi Dr. Lazarus Chakwera unamvana kuti a Chakwera adzalamulira zaka zisanu kenako adzapereka mpata kwa a Chilima kuti alamulirenso zaka zina zisanu.