Saturday, March 2, 2024
Local Malawi News

MUNTHARIKA APEMPHA MGWIRIZANO MU NTHAWI YA NAMONDWE

Mtsogoleri wachipani cha Democratic Progressive – DPP, Professor Peter Mutharika wapempha anthu komanso mabungwe m’dziko muno kuti agwirane manja pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi namondwe wa Freddy.

Izi ndi malingana ndichikalata chomwe a Mutharika atulutsa lero kudzera mwa m’neneri wawo a Shadreck Namalomba.

DPP leader Muntharika

A Mutharika omwe ndi mtsogoleri wakale wadziko lino ati ali ndi chisoni ndi anthu omwe afa, kuvulala komanso kutaya katundu wawo kudzera pangoziyi.

Apa iwo alangizanso anthu omwe ali kumalo omwe ali pachiopsezo cha ngozi kuti asamukire kumalo okwera komanso ayamikira mabungwe komanso anthu omwe ayambapo kale kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngoziyi.

Lolemba sabata ino, mtsogoleri wadziko lini Dr Lazarus Chakwera analengeza kuti maboma am’chigawo chakumwera kwadziko lino ali pa ngozi kaamba ka namondwe wa Freddy ndipo apempha mabungwe komanso anthu akufuna kwabwino kuti athandize anthu omwe akhudzidwa.

Pakadali pano anthu oposera 100 amwalira pomwe maanja oposera 10,000 akhudzidwa ndi namondwe wa Freddy.

(Visited 6 times, 1 visits today)
admin
the authoradmin
News Breeze Malawi is an independent online news portal which reports news from Malawi, Africa and elsewhere. Our reports are not opinionated and strictly follow the rules and laws of reporting in professional journalism. Contact - newsbreezemalawi@gmail.com

Leave a Reply